Genesis 50:13 - Buku Lopatulika13 chifukwa kuti ana ake aamuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 chifukwa kuti ana ake amuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Adamnyamula kupita ku Kanani, nakamuika m'phanga limene linali m'munda ku Makipera, kuvuma kwa Mamure. Abrahamu adagula phangalo kwa Efuroni Muhiti pamodzi ndi munda womwewo, kuti pakhale manda. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Ndiye kuti ana a Yakobo anamunyamula kupita naye ku Kanaani kuti akamuyike mʼphanga limene lili mʼmunda wa Makipela pafupi ndi Mamre. Abrahamu anagula mundawo kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda. Onani mutuwo |