Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 32:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndimyesera ndalama, masekeli khumi ndi asanu ndi awiri a siliva.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndimyesera ndalama, masekeli khumi ndi asanu ndi awiri a siliva.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Motero ndidagula mundawo ku Anatoti kwa Hanamele msuweni wanga, ndipo mtengo wake unali masekeli asiliva 17.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 choncho ndinagula munda wa ku Anatoti kwa Hanameli msuweni wanga, ndipo ndinamupatsa masekeli asiliva 17.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 32:9
11 Mawu Ofanana  

Ndipo panali zitatha kumwa ngamira, munthuyo anatenga mphete yagolide ya kulemera kwake sekeli latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ake, kulemera kwake masekeli khumi a golide.


Ndipo anapita pamenepo Amidiyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismaele ndi masekeli a siliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Ejipito.


Ndipo popitapo mfumu, anafuula kwa mfumu, nati, Kapolo wanu analowa pakati pa nkhondo, ndipo taonani, munthu anapatuka nabwera ndi munthu kwa ine, nati, Tasunga munthu uyu; akasowa ndi chifukwa chilichonse moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wake, kapena udzalipa talente la siliva,


Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.


Chikakomera mfumu, chilembedwe kuti aonongeke iwo; ndipo ndidzapereka matalente a siliva zikwi khumi m'manja a iwo akusunga ntchito ya mfumu, abwere nao kuwaika m'nyumba za chuma cha mfumu.


Ng'ombeyo ikatunga mnyamata kapena mdzakazi, azipatsa mbuye wake ndalama za masekeli a siliva makumi atatu, ndipo ng'ombeyo aiponye miyala.


Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona.


Ndipo chakudya chako uzichidya chiyesedwe masekeli makumi awiri tsiku limodzi; uzidyako tsiku ndi tsiku pa nthawi yake.


M'mwemo ndinadzigulira iye ndi masekeli khumi ndi asanu a siliva, ndi homeri ndi leteki wa barele;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa