Yeremiya 32:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Monga momwe Chauta adanenera, Hanamele msuweni wanga adadzandiwonadi ku bwalo la alonda. Iyeyo adati, ‘Gula munda wanga ku Anatoti m'dziko la Benjamini, poti iwe ndiye woyenera kuuwombola kuti ukhale choloŵa chako.’ Tsono ndidadziŵa kuti umenewu unali uthenga wa Chauta uja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Ndipo monga momwe Yehova ananenera, Hanameli, msuweni wanga anabweradi ku bwalo la alonda ndipo anati, “Gula munda wanga wa ku Anatoti mʼdziko la Benjamini. Popeza ndiwe woyenera kuwugula ndi kukhala wako, gula munda umenewu kuti ukhale wako.” “Ine ndinadziwa kuti amenewa anali mawu a Yehova aja; Onani mutuwo |