2 Samueli 14:26 - Buku Lopatulika26 Ndipo pometa tsitsi lake amameta potsiriza chaka, chifukwa tsitsi linamlemerera, chifukwa chake atalimeta anayesa tsitsi la pamutu wake, napeza masekeli mazana awiri, monga mwa muyeso wa mfumu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201426 Ndipo pometa tsitsi lake amameta potsiriza chaka, chifukwa tsitsi linamlemerera, chifukwa chake atalimeta anayesa tsitsi la pa mutu wake, napeza masekeli mazana awiri, monga mwa muyeso wa mfumu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa26 Chaka chilichonse ankameta tsitsi lake, chifukwa linkamlemera kwambiri. Ankati akalimeta Abisalomuyo, naliyesa pa sikelo tsitsilo, linkalemera makilogramu aŵiri, potsata muyeso wa mfumu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero26 Nthawi ina iliyonse akamameta tsitsi lake, ankameta pamene layamba kumulemera. Akatero amaliyeza, ndipo limalemera makilogalamu awiri pa sikelo yaufumu. Onani mutuwo |