Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 14:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo mu Israele monse munalibe wina anthu anamtama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pamutu wake mwa iye munalibe chilema.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo m'Israele monse munalibe wina anthu anamtama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pa mutu wake mwa iye munalibe chilema.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 M'dziko lonse la Israele panalibe munthu wina aliyense wokongola ndi wochititsa kaso ngati Abisalomu. Kuyambira kumapazi mpaka kumutu analibe chilema chilichonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Mʼdziko lonse la Israeli munalibe munthu amene anayamikidwa chifukwa cha maonekedwe ake wokongola ngati Abisalomu. Kuyambira kumutu mpaka ku mapazi ake, analibe chilema.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 14:25
11 Mawu Ofanana  

Ndipo atate wake sadamvute masiku ake onse, ndi kuti, Watero chifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu.


Natuluka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zilonda zowawa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pamutu pake.


Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.


Kuchokera pansi pa phazi kufikira kumutu m'menemo mulibe changwiro; koma mabala, ndi mikwingwirima, ndi zilonda; sizinapole, ngakhale kumangidwa, ngakhale kupakidwa mafuta.


omangira malamba m'chuuno mwao, ndi nduwira zazikulu zonyika pamitu pao, maonekedwe ao ngati akalonga onsewo, akunga a ku Babiloni, dziko la kubadwa kwao ndi Kasidi.


anyamata opanda chilema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ochenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'chinyumba cha mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Ababiloni.


Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.


kuti Iye akadziikire yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda chilema.


Yehova adzakukanthani ndi chilonda choipa chosachira nacho kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pamutu panu.


Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.


Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Saulo, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israele panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu ena onse anamlekeza m'chifuwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa