Eksodo 30:13 - Buku Lopatulika13 Ichi achipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri,) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo chopereka cha Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ichi achipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri,) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo chopereka cha Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Aliyense woyenera kulembedwa m'kalemberamo adzapereke theka la sekeli, ndiye kuti ndalama zolemera ngati magaramu asanu ndi limodzi, kutsata muyeso wa ku Nyumba ya Mulungu (paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi aŵiri). Ndalama zimenezi zidzakhala zopereka kwa Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Izi ndi zimene aliyense wolembedwa mu kawundula ayenera kupereka: theka la sekeli, kutanthauza ndalama zolemera magalamu asanu ndi limodzi malingana ndi kawerengedwe ka ndalama za ku Nyumba ya Mulungu. Paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi awiri. Theka la sekeli chidzakhala chopereka cha kwa Yehova. Onani mutuwo |