Eksodo 30:12 - Buku Lopatulika12 Pamene uwerenga ana a Israele, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Pamene uwerenga ana a Israele, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 “Ukamachita kalembera wa ana aamuna a Aisraele, munthu aliyense adzapereke kwa Chauta choombolera moyo wake, kuti mliri uliwonse usadzamugwere pamene kalemberayo akuchitika. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 “Pamene ukuchita kalembera wa Aisraeli, munthu aliyense ayenera kupereka kwa Yehova chowombolera moyo wake pamene akuwerengedwa. Motero mliri sudzabwera pa iwo pamene ukuwawerenga. Onani mutuwo |
kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la Yehova, ndilo mliri m'dzikomo, ndi mthenga wakuononga wa Yehova mwa malire onse a Israele. Ulingirire tsono, ndimbwezere mau anji Iye amene anandituma ine?