Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala?
Genesis 21:6 - Buku Lopatulika Ndipo Sara anati, Mulungu anandisekeretsa ine; onse akumva adzasekera pamodzi ndi ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Sara anati, Mulungu anandisekeretsa ine; onse akumva adzasekera pamodzi ndi ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Sara adati, “Mulungu wandikondweretsa ndi kundiseketsa. Aliyense amene adzamve zimenezi, adzakondwera nane.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sara anati, “Mulungu wandibweretsera mseko, ndipo aliyense amene adzamva zimenezi adzaseka nane pamodzi.” |
Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala?
Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; pamenepo anati kwa amitundu, Yehova anawachitira iwo zazikulu.
Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.
Pamenepo udzati m'mtima mwako, Ndani wandibalitsa ine amenewa, popeza ana anga anachotsedwa kwa ine, ndipo ndili wouma, ndi wochotsedwa m'dziko, ndi woyendayenda kwina ndi kwina? Ndipo ndani wadza ndi awa? Taona ndinasiyidwa ndekha, amenewa anali kuti?
Imba, iwe wouma, amene sunabale; imba zolimba ndi kufuula zolimba, iwe amene sunabale mwana; pakuti ana a mfedwa achuluka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.
Atembereredwe munthu amene anatengera mau kwa atate wanga, kuti, Mwana wamwamuna anakubadwira iwe; ndi kumsekeretsatu iye.
Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo anthu ambiri adzakondwera pa kubadwa kwake.
Ndipo anansi ake ndi abale ake anamva kuti Ambuye anakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi.
Ndi chikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yake, popeza anamwerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza;
Ndipo mkaziyo ananena, Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova.