1 Samueli 1:26 - Buku Lopatulika26 Ndipo mkaziyo ananena, Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201426 Ndipo mkaziyo ananena, Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa26 Tsono Hana adati, “Inu mbuyanga, ndikunenetsa kuti ndithudi ine ndine mkazi uja amene ndidaaimirira pano pamaso panu, ndikupemphera kwa Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero26 Ndipo Hana anati kwa Eli, “Mbuye wanga, ine ndikunenetsadi pamaso panu kuti ndine mkazi uja amene anayima pamaso panu ndi kumapemphera kwa Yehova. Onani mutuwo |
Ndipo mfumuyo inati, Kodi Yowabu adziwana ndi iwe mwa izi zonse? Mkaziyo nayankha nati, Pali moyo wanu mbuye wanga mfumu, palibe kulewa ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere kwa zonse mudazinena mbuye wanga mfumu; pakuti mnyamata wanu Yowabu ndiye anandiuza, naika mau onse awa m'kamwa mwa mdzakazi wanu.