Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nchiyani ichi wandichitira ine? Chifukwa chanji sunandiuze ine kuti ndiye mkazi wako?
Genesis 20:9 - Buku Lopatulika Ndipo Abimeleki anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Watichitira ife chiyani iwe? Ndakuchimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga uchimo waukulu? Wandichitira ine zosayenera kuzichita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abimeleki anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Watichitira ife chiyani iwe? Ndakuchimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga uchimo waukulu? Wandichitira ine zosayenera kuzichita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Abimeleki adaitana Abrahamu namufunsa kuti, “Kodi iwe watichita zotani? Kodi ine ndakulakwira chiyani, kuti iweyo undiputire chilango chotere ine ndi onse a mu ufumu wanga? Zimene wandichitazi nzosayenera konse kuzichita. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Abimeleki anayitana Abrahamu ndipo anati, “Kodi wachita chiyani? Ndakulakwira chiyani kuti undibweretsere ine pamodzi ndi anthu anga chilango chachikulu chotere? Wandichitira zinthu zimene sizinayenera kuchitika.” |
Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nchiyani ichi wandichitira ine? Chifukwa chanji sunandiuze ine kuti ndiye mkazi wako?
Ndipo Abimeleki analawira m'mamawa, naitana anyamata ake onse, nanena zonse zimenezo m'makutu mwao, ndipo anthu anaopa kwambiri
Ndipo Abimeleki anati, Nchiyani chimenechi watichitira ife? Panatsala pang'ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadatichimwitsa ife.
Ndipo panali m'mamawa, anaona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Chiyani wandichitira ine? Kodi sindinakutumikire iwe chifukwa cha Rakele? Wandinyenga ine bwanji?
Ndipo pakumva icho ana ake aamuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita.
Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wachita chigololo, ndiponso taonani, ali ndi pakati ndi chigololocho. Ndipo Yuda anati, Mtulutse iye kuti amponye pamoto.
mulibe wina m'nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?
Pamenepo mkwiyo wa Davide unayaka ndithu pa munthuyo, nati kwa Natani, Pali Yehova, munthu amene anachita ichi, ayenera kumupha;
Koma iye anamyankha nati, Iai, mlongo wanga, usandichepetsa ine, pakuti chinthu chotere sichiyenera kuchitika mu Israele, usachita kupusa kumeneku.
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere?
Wosocheretsa oongoka mtima alowe m'njira yoipa, adzagwa mwini m'dzenje lake; koma angwiro adzalandira cholowa chabwino.
Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri.
amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja banja lonse, ndi kuphunzitsa zosayenera chifukwa cha chisiriro chonyansa.
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.
Ndipo Yoswa anati, Watisautsiranji? Yehova adzakusautsa lero lino. Ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nawatentha ndi moto, nawaponya miyala.