Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 29:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo panali m'mamawa, anaona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Chiyani wandichitira ine? Kodi sindinakutumikire iwe chifukwa cha Rakele? Wandinyenga ine bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo panali m'mamawa, anaona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Chiyani wandichitira ine? Kodi sindinakutumikira iwe chifukwa cha Rakele? Wandinyenga ine bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 M'maŵa mwake kutacha, Yakobe adaona kuti mkaziyo ndi Leya. Tsono adafunsa Labani kuti, “Chifukwa chiyani mwandichita zotere? Kodi suja ndidakugwirirani ntchito kuti ndikwatire Rakele? Chifukwa chiyani tsono mwandinyenga?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Pakucha mmawa, Yakobo anaona kuti anagona ndi Leya. Choncho Yakobo anafunsa Labani, “Nʼchiyani mwandichitirachi? Kodi ine sindinakugwirireni ntchito chifukwa cha Rakele? Bwanji mwandinyenga?”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 29:25
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nchiyani ichi wandichitira ine? Chifukwa chanji sunandiuze ine kuti ndiye mkazi wako?


Ndipo Abimeleki anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Watichitira ife chiyani iwe? Ndakuchimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga uchimo waukulu? Wandichitira ine zosayenera kuzichita.


Ndipo Abimeleki anati, Nchiyani chimenechi watichitira ife? Panatsala pang'ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadatichimwitsa ife.


Ndipo Labani anali ndi ana aakazi awiri, dzina la wamkulu ndi Leya, dzina la wamng'ono ndi Rakele.


Ndipo Labani anampatsa mwana wake wamkazi Leya Zilipa mdzakazi wake kuti akhale mdzakazi wa Leya.


Ndipo Labani anati, Satero kwathu kuno, kupatsa wamng'ono asanapatse wamkulu.


Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Wachitanji? Wathawa kwa ine mobisika ndi kutenga ana anga aakazi, monga mikoli ya lupanga.


Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipiro anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andichitire ine choipa.


Taonani, wolungama adzalandira mphotho kunja kuno; koposa kotani woipa ndi wochimwa?


Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.


Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.


Ananena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva chisoni kuti anati kwa iye kachitatu, Kodi undikonda Ine? Ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.


ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.


Pamenepo anthu onse anali kuchipata, ndi akulu, anati, Tili mboni ife. Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israele, iwo awiri; nuchite iwe moyenera mu Efurata, numveke mu Betelehemu;


Ndipo mkaziyo pakuona Samuele, anafuula ndi mau aakulu; ndi mkaziyo analankhula ndi Saulo, nati, Munandinyengeranji? Popeza inu ndinu Saulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa