Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 13:12 - Buku Lopatulika

12 Koma iye anamyankha nati, Iai, mlongo wanga, usandichepetsa ine, pakuti chinthu chotere sichiyenera kuchitika mu Israele, usachita kupusa kumeneku.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Koma iye anamyankha nati, Iai, mlongo wanga, usandichepetsa ine, pakuti chinthu chotere sichiyenera kuchitika m'Israele, usachita kupusa kumeneku.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Koma Tamarayo adayankha kuti, “Iyai, mlongo wanga, usandikakamize. Zimenezi sizidachitikepo nkale lonse ku Israele. Usachite zauchitsiru zotere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Tamara anati kwa iye, “Ayi mlongo wanga! Usandikakamize. Zotere siziyenera kuchitika mu Israeli! Usachite chinthu choyipa chotere.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 13:12
12 Mawu Ofanana  

Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.


Ndipo pakumva icho ana ake aamuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita.


ndinazindikira pakati pa aang'ono mnyamata wopanda nzeru,


chifukwa anachita zopusa mu Israele, nachita chigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.


Usamavula mwana wamkazi wa mkazi wa atate wako, amene anambala atate wako, ndiye mlongo wako.


Usamavula mlongo wako, mwana wamkazi wa atate wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, wobadwa kwanu, kapena wobadwa kwina.


Munthu akatenga mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa mai wake, nakaona thupi lake, ndi mlongoyo akaona thupi lake; chochititsa manyazi ichi; ndipo awasadze pamaso pa ana a anthu ao; anavula mlongo wake; asenze mphulupulu yake.


pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mzinda wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa mu Israele, kuchita chigololo m'nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu.


pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wake wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wake; popeza anamchepetsa; sangathe kumchotsa masiku ake onse.


Ndipo munthu mwini nyumba anawatulukira nanena nao, Iai, abale anga, musachite choipa chotere; popeza mwamuna uyu walowa m'nyumba mwanga, musachite chopusa ichi.


Pamenepo ndinagwira mkazi wanga wamng'ono ndi kumgawa ndi kumtumiza m'dziko lonse la cholowa cha Israele, pakuti anachita chochititsa manyazi ndi chopusa mu Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa