Genesis 34:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo pakumva icho ana ake aamuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo pakumva icho ana ake amuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Pa nthaŵi imeneyo ana ake a Yakobewo anali atangobwerako kubusa kuja. Anawo atamva zimenezo, adapsa mtima kwambiri. Adakwiya koopsa poona kuti Sekemu wachita chinthu choipa kwambiri ndi kuchita chipongwe Aisraele, pogwira Dina, mwana wa Yakobe, nkuchita naye zoipa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Pa nthawi iyi nʼkuti ana a Yakobo atabwererako ku busa kuja. Iwo atangomva zimene zinachitika, anawawidwa mtima. Iwo anapsa mtima kwambiri kuti Sekemu nʼkuchita chonyansa choterechi mu dziko la Israeli, kumugwirira Dina, mwana wa Yakobo. Onani mutuwo |