Genesis 2:11 - Buku Lopatulika Dzina la woyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golide; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Dzina la wakuyamba Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golide; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtsinje woyamba ndi Pisoni, ndipo umayenda mozungulira dziko la Havila, kumene kumapezeka golide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzina la mtsinje woyamba ndi Pisoni; uwu umazungulira dziko lonse la Havila, kumene kuli golide. |
Ndi ana aamuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedani.
Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum'mawa kwake kwa Ejipito, pakunka ku Asiriya: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ake onse.
Efuremu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israele ndi chinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.
Ndipo Saulo anakantha Aamaleke, kuyambira pa Havila, dera la ku Suri, chili pandunji pa Ejipito.