Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 14:1 - Buku Lopatulika

Ndipo panali masiku a Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara, ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu,

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo panali masiku a Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara, ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu,

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Masiku amenewo, Amurafere mfumu ya ku Sinara, Ariyoki mfumu ya ku Elasara, Kedorilaomere mfumu ya ku Elamu, ndi Tidala mfumu ya ku Goimu,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pa nthawi imeneyi Amarafeli mfumu ya Sinara, Arioki mfumu ya Elasara, Kedorilaomere mfumu ya Elamu ndi Tidala mfumu ya Goimu

Onani mutuwo



Genesis 14:1
15 Mawu Ofanana  

Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.


Ana aamuna a Semu; Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu.


Ndipo panali pamene anayendayenda ulendo kum'mawa, anapeza chigwa m'dziko la Sinara, ndipo anakhala kumeneko.


ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu, ndi Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara; mafumu anai kumenyana ndi asanu.


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja.


Masomphenya ovuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Mediya iwe; kuusa moyo kwake konse ndakutonthoza.


Ndipo Elamu anatenga phodo, ndi magaleta a anthu ndi apakavalo; ndipo Kiri anaonetsa zikopa.


Kodi milungu ya amitundu yaipulumutsa iyo, imene atate anga anaipasula? Gozani ndi Harani ndi Rezefe ndi ana a Edeni amene anali mu Telasara.


ndi mafumu onse a Zimiri, ndi mafumu onse a Elamu, ndi mafumu onse a ku Mediya,


Elamu ali komwe ndi gulu lake lonse lozinga manda ake; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwake kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.


Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake.


Ndipo ndinaona m'masomphenya; tsono kunali, pakuwaona ine ndinali mu Susa, m'nyumba ya mfumu, ndiwo m'dziko la Elamu; ndinaona m'masomphenya kuti ndinali kumtsinje Ulai.


Ndipo anati kwa ine, Kummangira nyumba m'dziko la Sinara; kuti amuike efayo, namkhazikeko pamalo kwake.


mfumu ya ku Dori, mpaka ponyamuka pa Dori, imodzi; mfumu ya ku Goimu mu Galileya, imodzi;