Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 8:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo ndinaona m'masomphenya; tsono kunali, pakuwaona ine ndinali mu Susa, m'nyumba ya mfumu, ndiwo m'dziko la Elamu; ndinaona m'masomphenya kuti ndinali kumtsinje Ulai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo ndinaona m'masomphenya; tsono kunali, pakuwaona ine ndinali m'Susa, m'nyumba ya mfumu, ndiwo m'dziko la Elamu; ndinaona m'masomphenya kuti ndinali kumtsinje Ulai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndinaona mʼmasomphenya kuti ndinali mu mzinda wotetezedwa wa Susa mʼchigawo cha Elamu. Mʼmasomphenyawo ndinaona nditayima pafupi ndi mtsinje wa Ulai.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 8:2
24 Mawu Ofanana  

Ana aamuna a Semu; Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu.


Ndipo panali masiku a Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara, ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu,


Mau a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pokhala ine ku Susa kunyumba ya mfumu,


Masiku ajawo, pokhala Ahasuwero pa mpando wa ufumu wake uli m'chinyumba cha ku Susa,


Ndipo kunali, atamveka mau a mfumu ndi lamulo lake, ndipo atasonkhanidwa anamwali ambiri m'chinyumba cha ku Susa, awasunge Hegai, anamtenga Estere yemwe, alowe m'nyumba ya mfumu, amsunge Hegai wosunga akazi.


Amtokoma anatuluka ofulumizidwa ndi mau a mfumu, ndi lamulo linabukitsidwa m'chinyumba cha ku Susa; ndipo mfumu ndi Hamani anakhala pansi kumwa; koma mzinda wa Susa unadodoma.


Nati Estere, Munthu wosautsa ndi mdani ndiye Hamani woipa uyu. Pamenepo Hamani anagwidwa mantha pamaso pa mfumu ndi mkazi wamkulu.


Ndipo Mordekai anatuluka pamaso pa mfumu wovala chovala chachifumu chamadzi ndi choyera, ndi korona wamkulu wagolide, ndi malaya abafuta ndi ofiirira; ndi mzinda wa Susa unafuula ndi kukondwera.


Tsiku lomwelo anabwera nacho kwa mfumu chiwerengo cha iwo ophedwa m'chinyumba cha ku Susa.


Ndipo Ayuda okhala mu Susa anasonkhana pamodzi, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wa Adara, napha amuna mazana atatu mu Susa; koma sanalande zofunkha.


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja.


Masomphenya ovuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Mediya iwe; kuusa moyo kwake konse ndakutonthoza.


ndi mafumu onse a Zimiri, ndi mafumu onse a Elamu, ndi mafumu onse a ku Mediya,


Ndipo kunali chaka cha makumi atatu, mwezi wachinai, tsiku lachisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.


Elamu ali komwe ndi gulu lake lonse lozinga manda ake; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwake kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.


Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi woyamba, pokhala ine m'mphepete mwa mtsinje waukulu, ndiwo Tigrisi,


Koma ine Daniele, mzimu wanga unalaswa m'kati mwa thupi langa, ndi masomphenya a m'mtima mwanga anandivuta.


Daniele ananena, nati, Ndinaona m'masomphenya anga usiku, taonani, mphepo zinai za mumlengalenga zinabuka pa nyanja yaikulu.


Chaka chachitatu cha Belisazara mfumu masomphenya anandionekera kwa ine Daniele, atatha kundionekera oyamba aja.


Ndipo ndinakweza maso anga ndi kupenya; taonani, panaima pamtsinje nkhosa yamphongo yokhala nazo nyanga ziwiri, ndi nyanga ziwirizo zinali za msinkhu wautali, koma imodzi inaposa inzake; yoposayo inaphuka m'mbuyo.


Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.


Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana,


Ndipo kotero ndinaona akavalo m'masomphenya, ndi iwo akuwakwera akukhala nazo zikopa za moto, ndi huakinto ndi sulufure; ndi mitu ya akavalo ngati mitu ya mikango; ndipo m'kamwa mwao mutuluka moto ndi utsi ndi sulufure.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa