Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 13:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo Abramu anasuntha hema wake nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure, imene ili mu Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo Abramu anasuntha hema wake nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure, imene ili m'Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Motero Abramu adazula hema lake, nakakhala patsinde pa mitengo ya thundu ya ku Mamure, imene ili ku Hebroni. Ndipo kumeneko adamangira Chauta guwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Choncho Abramu anasamutsa tenti yake napita kukakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ija ya thundu ya ku Mamre ku Hebroni, kumene anamangira Yehova guwa lansembe.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 13:18
17 Mawu Ofanana  

kumalo kwa guwa la nsembe analimanga iye kumeneko, poyamba paja; ndipo pamenepo Abramu anaitanira dzina la Yehova.


Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.


Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamure, pamene anakhala pa khomo la hema wake pakutentha dzuwa.


Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isaki mwana wake, namuika iye paguwa la nsembe pamwamba pa nkhuni.


Ndipo Sara anafa mu Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.


Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, naitana dzina la Yehova, namanga hema wake kumeneko: ndi pamenepo anyamata a Isaki anakumba chitsime.


Ndipo Yakobo anafika kwa Isaki atate wake ku Mamure, ku Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni) kumene anakhala Abrahamu ndi Isaki.


Ndipo anati kwa iye, Pita tsopano, nukaone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta zili bwino; nundibwezere ine mau. Ndipo anamtuma iye kuchokera m'chigwa cha Hebroni, ndipo anadza ku Sekemu.


Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.


Ndipo zitatha izi Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndikwere kunka m'mizinda wina wa Yuda? Ndipo Yehova ananena naye, Kwera. Davide nanena naye, Ndikwere kuti? Ndipo anati, Ku Hebroni.


Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.


Ndipo anakwera njira ya kumwera nafika ku Hebroni; ndi apa panali Ahimani, Sesai, ndi Talimai, ana a Anaki. (Koma atamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri ndipo anamanga Zowani mu Ejipito.)


Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.


Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;


Pamenepo Yoswa anamdalitsa, napatsa Kalebe mwana wa Yefune Hebroni likhale cholowa chake.


Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa