Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa.
Genesis 12:5 - Buku Lopatulika Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala m'Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abramu adatenga mkazi wake Sarai, Loti mwana wa mng'ono wake, pamodzi ndi chuma chake chonse, ndi antchito amene adaali nawo ku Harani. Adayamba ulendo wonka ku Kanani. Atafika ku Kanani, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani. |
Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa.
Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harani; ndipo Harani anabala Loti.
Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harani, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldeya kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harani, nakhala kumeneko.
Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: chifukwa kuti chuma chao chinali chambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi.
Pamene anamva Abramu kuti mphwake anagwidwa, anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani.
Ndipo Esau anatenga akazi ake, ndi ana ake aamuna, ndi ana ake aakazi, ndi anthu onse a m'banja mwake, ndi ng'ombe zake, ndi zoweta zake, ndi zonse anali nazo anasonkhanitsa m'dziko la Kanani; ndipo ananka ku dziko losiyana patali ndi Yakobo mphwake.
Koma wansembe atakagula munthu ndi ndalama zake, iyeyu adyeko; ndi iwo amene anabadwa m'nyumba yake, adyeko mkate wake.
Pamenepo anatuluka m'dziko la Akaldeya namanga mu Harani: ndipo, kuchokera kumeneko, atamwalira atate wake, Mulungu anamsuntha alowe m'dziko lino, m'mene mukhalamo tsopano;