Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 13:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: chifukwa kuti chuma chao chinali chambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: chifukwa kuti chuma chao chinali chambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono dziko lodyetsapo zoŵeta linali losakwanira onse aŵiriwo, poti aliyense anali ndi zoŵeta zambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Motero dziko linayamba kuwachepera kuti onse nʼkukhala pamodzi, popeza katundu wawo anali wochuluka kwambiri moti sakanatha kukhala pamodzi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 13:6
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anamchitira Abramu bwino chifukwa cha iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi abulu aakazi, ndi ngamira.


Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.


Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng'ombe ndi siliva ndi golide.


Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m'chiyesero ndi m'msampha, ndi m'zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m'chionongeko ndi chitayiko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa