Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 13:5 - Buku Lopatulika

5 Ndiponso Loti anayenda ndi Abramu anali ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi mahema.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndiponso Loti anayenda ndi Abramu anali ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi mahema.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Loti nayenso amene ankayenda limodzi ndi Abramu, anali ndi nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe pamodzi ndi banja lake ndi antchito ake amene ankakhala naye limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Loti amene ankayendayenda ndi Abramu nayenso anali ndi ziweto zosiyanasiyana ndi matenti.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 13:5
6 Mawu Ofanana  

Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka mu Harani.


Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.


Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: chifukwa kuti chuma chao chinali chambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi.


Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziwa zakusaka nyama, munthu wa m'thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m'mahema.


Ndipo Ada anabala Yabala; iye ndiye atate wao wa iwo okhala m'mahema, akuweta ng'ombe.


Mahema ao ndi zoweta zao adzazilanda, adzadzitengera nsalu zotchingira zao, ndi katundu wao yense, ndi ngamira zao; ndipo adzafuulira iwo, Mantha ponseponse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa