Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 13:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo panali ndeu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti. Akanani ndi Aperizi ndipo analinkukhala nthawi yomweyo m'dzikomo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo panali ndeu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti: Akanani ndi Aperizi ndipo analinkukhala nthawi yomweyo m'dzikomo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Motero padaauka ndeu pakati pa abusa a Abramu ndi abusa a Loti. Nthaŵi imeneyo nkuti Akanani ndi Aperizi akadalipo m'dzikomo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mikangano inayambika pakati pa abusa a Abramu ndi abusa a Loti. Nthawi imeneyo nʼkuti Akanaani ndi Aperezi akukhalanso mʼdziko lomwelo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 13:7
20 Mawu Ofanana  

Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa.


Ndipo Abramu anapitirira m'dzikomo kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m'dzikomo nthawi yomweyo.


Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi, anyamata ake a Abimeleki anachilanda.


Ndipo abusa a Gerari anakangana ndi abusa a Isaki kuti, Madzi ndi athu; ndipo anatcha dzina la chitsimecho Eseke: chifukwa anakangana naye.


Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwandisautsa ndi kundinukhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperizi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.


Mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng'ombe chiyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m'dziko la Goseni; chifukwa abusa onse anyansira Aejipito.


Ndinatinso, Chinthu muchitachi si chokoma ai; simuyenera kodi kuyenda m'kuopa Mulungu wathu, chifukwa cha mnyozo wa amitundu, ndiwo adani athu?


Pamenepo anadza abusa nawapirikitsa; koma Mose anauka nawathandiza, namwetsa gulu lao.


Kuli ulemu kwa mwamuna kupewa ndeu; koma zitsiru zonse zimangokangana.


Ndipo nyumba ikagawanika pa iyo yokha, singathe kukhazikika nyumbayo.


pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?


kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko,


Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthawi ingatayike.


kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu.


Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.


Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali chisokonekero ndi chochita choipa chilichonse.


Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu?


ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa