Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 14:21 - Buku Lopatulika

21 Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge chuma iwe wekha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge chuma iwe wekha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Komanso mfumu ya ku Sodomu idapempha Abramu kuti “Zinthu zonse mudatengazi, musunge, koma anthu anga okhaŵa mundipatse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Mfumu ya Sodomu inati kwa Abramu, “Ine undipatse anthu okhawo, koma katundu akhale wako.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 14:21
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.


Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge thoo; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.


Ndipo anatenga chuma chonse cha Sodomu ndi Gomora ndi zakudya zao zonse, namuka.


ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.


Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi


Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za chakudya chanu, ndi cha ana anu ndi mabanja anu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa