Chifukwa chanji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nuchoke.
Genesis 12:18 - Buku Lopatulika Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nchiyani ichi wandichitira ine? Chifukwa chanji sunandiuze ine kuti ndiye mkazi wako? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nchiyani ichi wandichitira ine? Chifukwa chanji sunandiuza ine kuti ndiye mkazi wako? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Farao adaitana Abramu namufunsa kuti, “Kodi iwe, wandichita zotani? Bwanji osandiwuza kuti ameneyu ndi mkazi wako? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Farao anayitanitsa Abramu namufunsa kuti, “Nʼchiyani wandichitirachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiwuze kuti ameneyu ndi mkazi wako? |
Chifukwa chanji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nuchoke.
Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
Ndipo panali m'mamawa, anaona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Chiyani wandichitira ine? Kodi sindinakutumikire iwe chifukwa cha Rakele? Wandinyenga ine bwanji?
Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.
Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Wachitanji? Wathawa kwa ine mobisika ndi kutenga ana anga aakazi, monga mikoli ya lupanga.
Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ichi nchiyani mwachichita? Kodi simudziwa kuti munthu ngati ine ndingathe kuzindikira ndithu?
Pomwepo Yowabu anadza kwa mfumu, nati, Mwachitanji? Taonani, Abinere anadza kwa inu, chifukwa ninji tsono munalawirana naye kuti achokedi.
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere?
Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, uchitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israele, numlemekeze Iye; nundiuze tsopano, wachitanji? Usandibisire.
ndipo inu, musamachita pangano ndi nzika za m'dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvere mau anga; mwachichita ichi chifukwa ninji?
Pamenepo Saulo ananena ndi Yonatani, Undiuze chimene unachita. Ndipo Yonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo inali m'dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa.