Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 2:2 - Buku Lopatulika

2 ndipo inu, musamachita pangano ndi nzika za m'dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvere mau anga; mwachichita ichi chifukwa ninji?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 ndipo inu, musamachita pangano ndi nzika za m'dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvera mau anga; mwachichita ichi chifukwa ninji?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsono inuyo musadzachite chipangano ndi nzika za dziko lino. Mudzaphwanye maguwa ao onse.’ Koma inu simudamvere lamulo langa. Zimenezi mwachitiranji?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 ndipo inu musadzachite pangano ndi anthu a dziko lino, koma mudzaphwanye maguwa awo ansembe.’ Koma inu simunamvere lamulo langa. Chifukwa chiyani mwachita zimenezi?

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 2:2
29 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nchiyani ichi wandichitira ine? Chifukwa chanji sunandiuze ine kuti ndiye mkazi wako?


Ndipo anati, Wachita chiyani? Mau a mwazi wa mphwako andifuulira Ine kunthaka.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere?


Tsopano uli nacho chiyani m'njira ya ku Ejipito, kumwa madzi a mtsinje wa Nailo? Uli nacho chiyani m'njira ya ku Asiriya, kumwa madzi a mtsinje wa Yufurate?


Bwanji uyendayenda kwambiri ndi kusintha njira yako? Udzachitanso manyazi ndi Ejipito monga unachita manyazi ndi Asiriya.


atero Yehova, Atate anu apeza chosalungama chanji mwa Ine, kuti andichokera kunka kutali, natsata zachabe, nasanduka achabe?


Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawachitire chifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakuchitirani msampha.


m'lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu;


Ndipo amuna a Israele anati kwa Ahivi, Kapena mulimkukhala pakati pa ife, ndipo tipanganenji ndi inu?


Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani?


Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele; nati Iye, Popeza mtundu uwu unalakwira chipangano changa chimene ndinalamulira makolo ao, osamvera mau anga;


ndipo ndinati kwa inu, Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musamaopa milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma simunamvere mau anga.


Yehova anatuma munthu mneneri kwa ana a Israele, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ine ndinakukwezani kuchokera mu Ejipito, ndi kukutulutsani m'nyumba ya ukapolo;


Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m'mzinda mwake, ndiwo Ofura; ndi Israele yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yake ngati msampha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa