1 Samueli 14:43 - Buku Lopatulika43 Pamenepo Saulo ananena ndi Yonatani, Undiuze chimene unachita. Ndipo Yonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo inali m'dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201443 Pamenepo Saulo ananena ndi Yonatani, Undiuze chimene unachita. Ndipo Yonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo inali m'dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa43 Apo Saulo adauza Yonatani kuti, “Tandiwuza zimene wachita.” Yonatani adauza bambo wakeyo kuti, “Ndidalaŵako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo yanga. Ndiye ai, chomwecho, ine ndili wokonzeka kuti ndife.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero43 Kenaka Sauli anati kwa Yonatani, “Ndiwuze chimene wachita.” Ndipo Yonatani anamuwuza kuti, “Ine ndinangolawa uchi pangʼono ndi ndodo yangayi. Ndiye ine ndili wokonzeka kufa.” Onani mutuwo |