Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 11:8 - Buku Lopatulika

Ndipo Yehova anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi, ndipo analeka kumanga mzinda.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi, ndipo analeka kumanga mudzi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Motero Chauta adaŵamwaza anthuwo pa dziko lonse lapansi, ndipo iwowo adaleka kumanga mzindawo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo.

Onani mutuwo



Genesis 11:8
10 Mawu Ofanana  

Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana aamuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m'masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani.


Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu padziko lapansi, chitapita chigumula.


Amenewo ndipo anagawa zisumbu za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.


Ndipo anati, Tiyeni, timange mzinda ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi.


Chifukwa chake anatcha dzina lake Babiloni pakuti kumeneko Yehova anasokoneza chinenedwe cha dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi.


Kutembereredwe kukwiya kwao, chifukwa kunali koopsa; ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe. Ndidzawagawanitsa mu Yakobo. Ndidzabalalitsa iwo mu Israele.


Yehova aphwanya upo wa amitundu, asandutsa chabe zolingirira za mitundu ya anthu.


Pakuti, taonani, adani anu, Yehova, pakuti, taonani, adani anu adzatayika; ochita zopanda pake onse adzamwazika.


Iye anachita zamphamvu ndi mkono wake; Iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wao.


Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu cholowa chao, pamene anagawa ana a anthu, anaika malire a mitundu ya anthu, monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israele.