Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 10:5 - Buku Lopatulika

5 Amenewo ndipo anagawa zisumbu za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Amenewo ndipo anagawa zisi za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Iwoŵa ndiwo anali makolo a onse amene ankakhala m'mbali mwa nyanja, ndi pa zilumba zam'nyanja. Ameneŵa ndiwo ana a Yafeti. Mafuko ao anali osiyanasiyana, ndipo ankakhala m'maiko osiyanasiyana. Fuko lililonse linkalankhula chilankhulo chakechake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 (Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).

Onani mutuwo Koperani




Genesis 10:5
26 Mawu Ofanana  

Amenewa ndi ana aamuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.


Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana aamuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m'masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani.


Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu padziko lapansi, chitapita chigumula.


Ndi ana aamuna a Yavani: Elisa, ndi Tarisisi, ndi Kitimu, ndi Dodanimu.


Ndi ana aamuna a Hamu: Kusi, ndi Ejipito, ndi Puti, ndi Kanani.


Amenewa ndiwo ana aamuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi.


Ndipo mfumu Ahasuwero inasonkhetsa dziko, ndi zisumbu za ku nyanja.


Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja.


Chifukwa chake lemekezani inu Yehova kum'mawa, ngakhale dzina la Yehova, Mulungu wa Israele, m'zisumbu za m'nyanja.


Taonani, amitundu akunga dontho la m'mtsuko, nawerengedwa ngati fumbi losalala la m'muyeso; taonani atukula zisumbu ngati kanthu kakang'ono.


Zisumbu zinaona ndipo zinaopa; malekezero a dziko lapansi ananthunthumira; anayandikira, nafika.


Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse zili m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.


Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa chiweruzo m'dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira chilamulo chake.


Mverani Ine, zisumbu inu, mumvere anthu inu akutali; Yehova anandiitana Ine ndisanabadwe; m'mimba mwa amai Iye anatchula dzina langa;


Chilungamo changa chili pafupi, chipulumutso changa chamuka; ndipo mikono yanga idzaweruza anthu; zisumbu zidzandilindira, ndipo adzakhulupirira mkono wanga.


Monga mwa ntchito zao momwemo Iye adzabwezera amaliwongo ake ukali, nadzabwezera adani ake chilango; nadzabwezeranso zisumbu chilango.


Zoonadi, zisumbu zidzandilindira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisisi kutenga ana ako aamuna kutali, golide wao ndi siliva wao pamodzi nao, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele, popeza Iye wakukometsa iwe.


Pakuti pitani ku zisumbu za Kitimu nimuone; tumizani ku Kedara nimulingalire bwino; nimuone ngati chinalipo chotere.


ndi mafumu onse a Tiro, ndi mafumu onse a Sidoni, ndi mafumu a chisumbu chimene chili patsidya pa nyanja;


Atero Ambuye Yehova kwa Tiro, Zisumbu sizidzagwedezeka nanga pomveka kugwa kwako, pobuula olasidwa, pakuchitika kuphako pakati pako?


Pamenepo zisumbu zidzanjenjemera tsiku la kugwa kwako, inde zisumbu za kunyanja zidzatenga nkhawa pa kuchokera kwako.


Pambuyo pake adzatembenuzira nkhope yake kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina adzaleketsa kunyoza kwake adanyoza nako; inde adzambwezera yekha kunyoza kwake.


Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya padziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pake, a m'zisumbu zonse za amitundu.


Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu cholowa chao, pamene anagawa ana a anthu, anaika malire a mitundu ya anthu, monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa