Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 33:10 - Buku Lopatulika

10 Yehova aphwanya upo wa amitundu, asandutsa chabe zolingirira za mitundu ya anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Yehova aphwanya upo wa amitundu, asandutsa chabe zolingirira za mitundu ya anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Zolinga za anthu akunja Chauta amazisandutsa zopandapake. Maganizo ao onse amaŵasandutsa achabechabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Yehova amalepheretsa chikonzero cha anthu a mitundu ina; Iye amaphwanya zolinga za anthu ambiri.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 33:10
23 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi, ndipo analeka kumanga mzinda.


Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.


koma ukabwerera kumzinda, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofele.


Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.


Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.


Ndipo munthu wa Mulunguyo anatuma mau kwa mfumu ya Israele, ndi kuti, Muchenjere musapite pakuti, popeza Aaramu alikutsikira uko.


Koma tinapemphera kwa Mulungu wathu, ndi kuwaikira olindirira usana ndi usiku, chifukwa cha iwowa.


Yehova, musampatse woipa zokhumba iye; musamthandize zodzipanga zake; angadzikuze.


Pakuti anakupangirani choipa, anapangana chiwembu, osakhoza kuchichita.


Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba, lakodwa phazi lao muukonde anautchera.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Ndipo mzimu wa Ejipito adzakhala wachabe pakati pake; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wake; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta.


Imbani m'mwamba inu, pakuti Yehova wachichita icho; kuwani inu, mbali za pansi padziko; imbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m'menemo; chifukwa kuti Yehova wapulumutsa Yakobo, ndipo adzadzilemekezetsa yekha mwa Israele.


Ndine amene nditsutsa zizindikiro za matukutuku, ndi kuchititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m'mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zao:


Ndipo ndidzataya uphungu wa Yuda ndi wa Yerusalemu m'malo ano; ndipo ndidzagwetsa iwo ndi lupanga pamaso pa adani ao, ndi padzanja la iwo amene afuna moyo wao; mitembo yao ndidzapatsa ikhale chakudya cha mbalame za m'mlengalenga, ndi cha zilombo za dziko lapansi.


ndi ichi chimauka mumtima mwanu sichidzachitika, umo mukuti, Tidzakhala ngati amitundu, ngati mabanja a m'maiko, kutumikira mtengo ndi mwala.


Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa