Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 49:7 - Buku Lopatulika

7 Kutembereredwe kukwiya kwao, chifukwa kunali koopsa; ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe. Ndidzawagawanitsa mu Yakobo. Ndidzabalalitsa iwo mu Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Kutembereredwe kukwiya kwao, chifukwa kunali koopsa; ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe. Ndidzawagawanitsa m'Yakobo. Ndidzabalalitsa iwo m'Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Matemberero aŵagwere, chifukwa mkwiyo wao ndi woopsa kwambiri, ukali wao utembereredwenso, chifukwa imeneyo ndi nkhalwe. Ndidzaŵamwaza iwowo m'dziko lonse la Yakobe. Ndidzaŵabalalitsa pakati pa Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Matemberero awagwere chifukwa cha mkwiyo wawo woopsa chonchi ndi ukali wawo wankhanza choterewu! Ine ndidzawabalalitsa mʼdziko la Yakobo ndi kuwamwaza iwo mʼdziko la Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 49:7
11 Mawu Ofanana  

Atatero Aminoni anadana naye ndi chidani chachikulu kopambana; pakuti chidani chimene anamuda nacho, chinali chachikulu koposa chikondi adamkonda nacho. Ndipo Aminoni ananena naye, Nyamuka, choka.


Ndipo anapatsa mwamaere, motapa pa fuko la ana a Yuda, ndi pa fuko la Simeoni, ndi pa fuko la ana a Benjamini, mizinda iyi yotchulidwa maina ao.


Mwala ulemera, mchenga ndiwo katundu; koma mkwiyo wa chitsiru upambana kulemera kwake.


Mwamuna wamkwiyo aputa makangano; waukali achuluka zolakwa.


Ndipo kunena za mizindayo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako mizinda yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa