Genesis 1:24 - Buku Lopatulika Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Mulungu adati, “Padziko pakhale mitundu yonse ya zamoyo potsata mitundu yake: zoŵeta, zokwaŵa, ndi nyama zakuthengo, potsata mitundu yake.” Ndipo zidachitikadi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Mulungu anati, “Dziko lapansi litulutse zolengedwa zamoyo monga mwa mitundu yawo: ziweto, zolengedwa zokwawa ndi nyama zakuthengo, iliyonse monga mwa mtundu wake.” Ndipo zinaterodi. |
Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazitcha; ndipo maina omwe onse anazitcha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao.
Za mbalame monga mwa mitundu yao, ndi zinyama monga mwa mitundu yao, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ziwiriziwiri monga mwa mitundu yao, zidzadza kwa iwe kuti zikhale ndi moyo.
iwo, ndi zamoyo zonse monga mwa mitundu yao, ndi zinyama zonse monga mwa mitundu yao, zokwawa zonse zokwawa padziko lapansi monga mwa mitundu yao, ndi zouluka zonse monga mwa mitundu yao, ndi mbalame zonse za mitundumitundu.
zinyama zonse, zokwawa zonse, zouluka zonse, ndi zonse zokwawa padziko lapansi, monga mwa mitundu yao, zinatuluka m'chingalawamo.