Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Filemoni 1:24 - Buku Lopatulika

ateronso, Marko, Aristariko, Dema, Luka, antchito anzanga.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ateronso, Marko, Aristariko, Dema, Luka, antchito anzanga.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Akutinso moni anzanga antchito, Marko, Aristariko, Dema, ndi Luka.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Atumiki anzanga awa, Marko, Aristariko, Dema ndi Luka, akuperekanso moni.

Onani mutuwo



Filemoni 1:24
15 Mawu Ofanana  

Ndipo m'mene adalingirirapo, anadza kunyumba ya Maria amake wa Yohane wonenedwanso Marko; pamenepo ambiri adasonkhana pamodzi, ndipo analikupemphera.


Ndipo Barnabasi ndi Saulo anabwera kuchokera ku Yerusalemu m'mene adatsiriza utumiki wao, natenga Yohane wonenedwanso Marko amuke nao.


Ndipo atamasula kuchokera ku Pafosi a ulendo wake wa Paulo anadza ku Perga wa ku Pamfiliya; koma Yohane anapatukana nao nabwerera kunka ku Yerusalemu.


Ndipo m'mzinda monse munachita piringupiringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristariko, anthu a ku Masedoniya, alendo anzake a Paulo.


Ndipo m'mene tidalowa m'ngalawa ya ku Adramitio ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, tinakankha, ndipo Aristariko Mmasedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe.


Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Khristu.


Koma ndinayesa nkofunika kutuma kwa inu Epafrodito mbaleyo, ndiye wantchito mnzanga ndi msilikali mnzanga, ndiye mtumwi wanu, ndi wonditumikira pa chosowa changa;


Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m'goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klemensinso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina ao ali m'buku la Moyo.


Aristariko wam'ndende mnzanga akupatsani moni, ndi Marko, msuweni wa Barnabasi (amene munalandira zolamulira za kwa iye; akafika kwanu, mumlandire iye),


Akupatsani moni Luka sing'anga wokondedwa, ndi Dema.


Iye wa ku Babiloni wosankhidwa pamodzi nanu akukupatsani moni; ateronso Marko mwana wanga.


Chifukwa chake ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana nacho choonadi.