Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 13:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo atamasula kuchokera ku Pafosi a ulendo wake wa Paulo anadza ku Perga wa ku Pamfiliya; koma Yohane anapatukana nao nabwerera kunka ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo atamasula kuchokera ku Pafosi a ulendo wake wa Paulo anadza ku Perga wa ku Pamfiliya; koma Yohane anapatukana nao nabwerera kunka ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Paulo ndi anzake adayenda m'chombo kuchokera ku Pafosi kukafika ku Perga m'dera la Pamfiliya. Koma Yohane adaŵasiya nabwerera ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Kuchokera ku Pafo, Paulo ndi anzake anayenda pa sitima ya pamadzi kupita ku Perga wa ku Pamfiliya, kumeneko Yohane anawasiya nabwerera ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 13:13
10 Mawu Ofanana  

Ndipo m'mene adalingirirapo, anadza kunyumba ya Maria amake wa Yohane wonenedwanso Marko; pamenepo ambiri adasonkhana pamodzi, ndipo analikupemphera.


Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerere, tizonde abale m'mizinda yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.


Koma sikunamkomere Paulo kumtenga iye amene anawasiya nabwerera pa Pamfiliya paja osamuka nao kuntchito.


mu Frijiya, ndiponso mu Pamfiliya, mu Ejipito, ndi mbali za Libiya wa ku Kirene, ndi alendo ochokera ku Roma,


Ndipo poomba pang'ono mwera, poyesa kuti anaona chofunirako, anakoka nangula, napita m'mbali mwa Krete.


Ndipo pamene tidapyola nyanja ya kunsi kwake kwa Silisiya ndi Pamfiliya, tinafika ku Mira wa Likiya.


Aristariko wam'ndende mnzanga akupatsani moni, ndi Marko, msuweni wa Barnabasi (amene munalandira zolamulira za kwa iye; akafika kwanu, mumlandire iye),


Luka yekha ali pamodzi ndi ine. Umtenge Marko, adze pamodzi ndi iwe; pakuti ayenera kunditumikira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa