Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 29:2 - Buku Lopatulika

ndi mkate wopanda chotupitsa, ndi timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndi mkate wopanda chotupitsa, ndi timitanda topanda chotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Utengenso buledi wosafufumitsa, makeke osatupitsa, osakaniza ndi mafuta, ndiponso mitanda ya buledi yopsapsalala yopaka mafuta. Zimenezi uzipange ndi ufa wosalala watirigu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Utengenso buledi wopanda yisiti, makeke wopanda yisiti wopakidwa mafuta. Zonsezi uzipange ndi ufa wosalala wa tirigu.

Onani mutuwo



Eksodo 29:2
14 Mawu Ofanana  

Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yoocha pamoto, ndi mkate wopanda chotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa.


ndi mkate wamphumphu umodzi, ndi kamtanda ka mkate wosakaniza ndi mafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, zili mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova;


Ndipo uziike mu dengu limodzi, ndi kubwera nazo mudengu, pamodzi ndi ng'ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.


Ndipo uthirepo mafuta, ndi kuikapo lubani; ndiyo nsembe yaufa.


Moto uziyakabe paguwa la nsembe, wosazima.


Ndipo nsembe zonse zaufa zosakaniza ndi mafuta, kapena zouma zikhale za ana onse a Aroni, alandireko onse.


akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tootcha, ta ufa wosalala tosakaniza ndi mafuta.


Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;


ndipo mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova, anatengeramo kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa, ndi kamtanda kamodzi ka mkate wamafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, natiika pa mafutawo, ndi pa mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;


ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa, timitanda ta ufa wosalala tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi todzoza ndi mafuta, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira.


Ndipo wansembe atenge mwendo wammwamba wophika wa nkhosa yamphongo, ndi kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa ka m'dengu, ndi kamtanda kaphanthi kopanda chotupitsa kamodzi, ndi kuziika m'manja mwa Mnaziri, atameta kusala kwake;


Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paska wathu waphedwa, ndiye Khristu;