Levitiko 7:12 - Buku Lopatulika12 akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tootcha, ta ufa wosalala tosakaniza ndi mafuta. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, timitanda topanda chotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tootcha, ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 akaipereka chifukwa cha kuthokoza, pamodzi ndi nsembe yothokozerayo apereke makeke osafufumitsa, osakaniza ndi mafuta, timitanda ta buledi wosafufumitsa, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wosakaniza bwino ndi mafuta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 “ ‘Ngati munthuyo apereka chifukwa cha kuthokoza, apereke nsembeyo pamodzi ndi makeke wopanda yisiti, osakaniza ndi mafuta; timitanda ta buledi wopanda yisiti, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wophikidwa bwino, wosakaniza ndi mafuta. Onani mutuwo |
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.