Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 8:2 - Buku Lopatulika

2 Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Utenge Aroni ndi ana ake. Utengenso zovala, mafuta odzozera, ng'ombe yamphongo ya nsembe yopepesera machimo, nkhosa ziŵiri zamphongo, ndipo utengenso dengu la buledi wosafufumitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Tenga Aaroni ndi ana ake, zovala zawo, mafuta wodzozera, ngʼombe yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, nkhosa ziwiri zazimuna ndi dengu la buledi wopanda yisiti,

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 8:2
15 Mawu Ofanana  

Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.


Ndipo usokere ana a Aroni malaya am'kati, nuwasokere mipango; uwasokerenso akapa akhale aulemerero ndi okoma.


zovala zokoma za kutumikira nazo m'malo opatulika, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, kuchita nazo ntchito ya nsembe.


Ndipo wansembe avale mwinjiro wake wabafuta, navale pathupi pake zovala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, moto utanyeketsa nsembe yamoto paguwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza chihema, ndi zonse zili m'mwemo, nazipatula.


Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo.


Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo yinayo, ndiyo mphongo ya kudzaza manja; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu wa mphongoyo.


nusonkhanitse khamu lonse ku khomo la chihema chokomanako.


amene alibe chifukwa cha kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyambira chifukwa cha zoipa za iwo eni, yinayi chifukwa cha zoipa za anthu; pakuti ichi anachita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa