Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 8:3 - Buku Lopatulika

3 nusonkhanitse khamu lonse ku khomo la chihema chokomanako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 nusonkhanitse khamu lonse ku khomo la chihema chokomanako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono usonkhanitse mpingo wonse pa khomo la chihema chamsonkhano.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 ndipo usonkhanitse gulu la anthu pa khomo la tenti ya msonkhano.”

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 8:3
16 Mawu Ofanana  

M'mwemo Davide anamemeza Aisraele onse kuyambira Sihori wa ku Ejipito mpaka polowera ku Hamati, kutenga likasa la Mulungu ku Kiriyati-Yearimu.


Ndipo Davide anasonkhanitsira Aisraele onse ku Yerusalemu, akwere nalo likasa la Yehova kumalo kwake adalikonzera.


Nasonkhana ku Yerusalemu anthu ambiri kuchita chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa mwezi wachiwiri, msonkhano waukulu ndithu.


Pakuti mfumu idapangana ndi akulu ake, ndi msonkhano wonse wa mu Yerusalemu, kuti achite Paska mwezi wachiwiri.


Ndi msonkhano wonse wa Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, ndi msonkhano wonse wochokera kwa Israele, ndi alendo ochokera kudziko la Israele, ndi okhala mu Yuda, anakondwera.


Pamenepo Solomoni anasonkhanitsira akuluakulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, ndi akalonga a nyumba za makolo a ana a Israele, ku Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova kumzinda wa Davide ndiwo Ziyoni.


Ndi mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Israele losonkhana kwa iye anali kulikasa, naphera nsembe, nkhosa ndi ng'ombe zosawerengeka kuchuluka kwake.


Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi kukhwalala lili ku Chipata cha Madzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la chilamulo cha Mose, chimene Yehova adalamulira Israele.


Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.


Ndipo wansembe amene amyeretsayo, amuike munthu uja wakuti ayeretsedwe, ndi zinthu zija, pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako;


Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;


Ndipo Mose anachita monga Yehova anamuuza; ndi khamulo linasonkhana pa khomo la chihema chokomanako.


Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwatulutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao.


Ndipo atachokapo anamuka ku Beere, ndicho chitsime chimene Yehova anachinena kwa Mose, Sonkhanitsa anthu, ndipo ndidzawapatsa madzi.


Ndipo ubwere nao Alevi pakhomo pa chihema chokomanako; nuwasonkhanitse khamu lonse la ana a Israele;


Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pamalo amodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa