Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 8:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta adauza Mose kuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova anawuza Mose kuti,

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 8:1
12 Mawu Ofanana  

Koma Aroni ndi ana ake ankafukiza paguwa la nsembe yopsereza, ndi paguwa la nsembe yofukiza, chifukwa cha ntchito yonse ya malo opatulika kwambiri, ndi kuchitira Israele chowatetezera, monga mwa zonse Mose mtumiki wa Mulungu adawauza.


Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.


Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.


Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andichitire Ine ntchito ya nsembe.


Ichi ndicho uwachitire kuwapatula, andichitire ntchito ya nsembe: tenga ng'ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro,


Ndipo zovala zopatulika za Aroni zikhale za ana ake aamuna pambuyo pake, kuti awadzoze atazivala, nadzaze manja ao atazivala;


Uwamangirenso Aroni ndi ana ake aamuna mipango m'chuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ake aamuna.


Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo.


Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake aamuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa ndi madzi.


chimene Yehova analamulira Mose m'phiri la Sinai, tsikuli anauza ana a Israele abwere nazo zopereka zao kwa Yehova, m'chipululu cha Sinai.


Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;


Awa ndi maina a ana aamuna a Aroni, ansembe odzozedwawo, amene anawadzaza manja ao achite ntchito ya nsembe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa