Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 6:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo wansembe atenge mwendo wammwamba wophika wa nkhosa yamphongo, ndi kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa ka m'dengu, ndi kamtanda kaphanthi kopanda chotupitsa kamodzi, ndi kuziika m'manja mwa Mnaziri, atameta kusala kwake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo wansembe atenge mwendo wamwamba wophika wa nkhosa yamphongo, ndi kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa ka m'dengu, ndi kamtanda kaphanthi kopanda chotupitsa kamodzi, ndi kuziika m'manja mwa Mnaziri, atameta kusala kwake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Tsono wansembe atenge mwendo wamwamba wa nkhosa yamphongo wophika, ndipo atengenso keke imodzi yosatupitsidwa, pamodzi ndi mtanda umodzi wa buledi wosatupitsidwa, ndipo aziike m'manja mwa Mnaziri, atameta tsitsi lake loperekedwa lija.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 “Mnaziriyo atatha kumeta tsitsi analiperekalo, wansembe ayike mʼmanja mwake mwendo wa mmwamba wankhosa yayimuna umene waphikidwa ndipo atengenso keke ndi kamtanda ka buledi, zonse zopanda yisiti zomwe zili mʼdengu lija.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 6:19
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


adze nazo m'manja mwake nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.


anaika zonsezi m'manja mwa Aroni, ndi m'manja mwa ana ake aamuna, naziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.


Ndipo Mose anati kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna, Phikani nyamayi pakhomo pa chihema chokomanako; ndipo muidyere komweko ndi mkate uli mu dengu la nsembe zodzaza manja, monga ndinauza, ndi kuti, Aroni ndi ana ake aidye.


Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mwamuna kapena mkazi akadzipatulira kulonjeza chowinda cha Mnaziri, kudzipatulira kwa Yehova;


Ngakhale asanayambe kupsereza mafuta, amadza mnyamata wa wansembe, namuuza wopereka nsembe, nati, Umpatse wansembeyo nyama yoti akaotche; pakuti safuna nyama yako yophika koma yaiwisi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa