Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 6:18 - Buku Lopatulika

18 Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wake wa kusala kwake pa khomo la chihema chokomanako, natenge tsitsi la pamutu wake wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wake wa kusala kwake pa khomo la chihema chokomanako, natenge tsitsi la pa mutu wake wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Mnaziriyo amete kumutu kwake koperekedwa kuja pakhomo pa chihema chamsonkhano. Ndipo atenge tsitsi la ku mutu wake woperekedwawo, ndi kulitentha pa moto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 “Mnaziriyo amete tsitsi limene analipereka lija pa khomo la tenti ya msonkhano. Atenge tsitsilo ndi kuliyika pa moto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 6:18
9 Mawu Ofanana  

naphe nkhosa yamphongo yoyamika ya Yehova, pamodzi ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa; wansembe akonzenso nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.


Masiku onse a chowinda chake chakusala, lumo lisapite pamutu pake; kufikira adatha masikuwo adadzipatulira kwa Yehova, azikhala wopatulika; aleke nzera za tsitsi lake zimeretu.


Munthu akafa chikomo pali iye, ndipo akadetsa mutu wake wowinda; pamenepo azimeta mutu wake tsiku la kumyeretsa kwake, tsiku lachisanu ndi chiwiri aumete.


Chotero inunso m'mene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.


Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, anatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m'ngalawa ku Siriya, pamodzi naye Prisila ndi Akwila; popeza anameta mutu wake mu Kenkrea; pakuti adawinda.


Chifukwa chake uchite ichi tikuuza iwe; tili nao amuna anai amene anawinda;


amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kuti amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzachabe, koma kuti iwe wekhanso uyenda molunjika, nusunga chilamulo.


Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m'mawa mwake m'mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa mu Kachisi, nauza chimalizidwe cha masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.


kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake, chimene anatichitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa