Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 6:15 - Buku Lopatulika

15 ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa, timitanda ta ufa wosalala tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi todzoza ndi mafuta, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa, timitanda ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi todzoza ndi mafuta, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Aperekenso dengu la buledi wosafufumitsa, makeke a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, timitanda ta buledi wosafufumitsa topyapyala ndi topaka mafuta, pamodzi ndi zopereka zake za zakudya ndi zachakumwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 ndipo abwere pamodzi ndi nsembe yachakudya ndi nsembe yachakumwa ndi dengu la buledi wopanda yisiti, makeke opangidwa ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda ta buledi topakidwa mafuta.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 6:15
15 Mawu Ofanana  

ndi mkate wopanda chotupitsa, ndi timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu.


koma iwo amene adzakolola adzadya ndi kutamanda Yehova; ndi iwo amene adzamtchera adzamumwa m'mabwalo a Kachisi wanga.


Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.


Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka kunyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, achita maliro.


Kaya, kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pake, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yothira ya Yehova Mulungu wanu.


Ndipo ukabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa, yophika mumchembo, chizikhala cha timitanda ta ufa wosalala topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, kapena timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta.


akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tootcha, ta ufa wosalala tosakaniza ndi mafuta.


Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;


ndi ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo zikhale zakuyamika, kuziphera nsembe pamaso pa Yehova; ndi nsembe yaufa yosakaniza ndi mafuta; pakuti lero Yehova wakuonekerani inu.


Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira limodzi la magawo awiri la hini, ndiye nsembe yamoto ya fungo lokoma, ya Yehova.


Ndipo wansembe azibwera nazo pamaso pa Yehova, nakonze nsembe yake yauchimo, ndi nsembe yake yopsereza;


Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.


Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa