Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 6:14 - Buku Lopatulika

14 pamenepo abwere nacho chopereka chake kwa Yehova, nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi yopanda chilema, ikhale nsembe yopsereza, ndi nkhosa yaikazi yopanda chilema ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema ikhale nsembe yoyamika;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 pamenepo abwere nacho chopereka chake kwa Yehova, nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi yopanda chilema, ikhale nsembe yopsereza, ndi nkhosa yaikazi yopanda chilema ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema ikhale nsembe yoyamika;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 ndipo iye apereke mphatso zake kwa Chauta. Apereke mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi wopanda chilema, kuti akhale nsembe yopsereza. Apereke nkhosa imodzi yaikazi ya chaka chimodzi yopanda chilema, kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, ndi nkhosa imodzi yamphongo yopanda chilema, kuti ikhale nsembe yachiyanjano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Pamenepo apereke chopereka chake kwa Yehova: Nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi yopanda chilema kuti ikhale nsembe yopsereza, mwana wankhosa wamkazi mmodzi wopanda chilema kuti ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa imodzi yayikulu yayimuna kuti ikhale nsembe yachiyanjano,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 6:14
12 Mawu Ofanana  

Ndipo popeza Mulungu anathandiza Alevi akusenza likasa la chipangano la Yehova, iwo anapha nsembe ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.


Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona, pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa; ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi.


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge anaankhosa awiri, amuna opanda chilema, ndi mwanawankhosa mmodzi wamkazi wa chaka chimodzi wopanda chilema, ndi atatu a magawo khumi a efa la ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa magawo atatu wa mafuta.


Ndipo chopereka chake chikakhala nkhosa kapena mbuzi, kuti ikhale nsembe yoyamika ya kwa Yehova; ingakhale yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema;


Ndipo akachimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, napalamula;


Ndipo akadza nayo nkhosa, ndiyo chopereka chake, ikhale nsembe yauchimo, azidza nayo yaikazi, yopanda chilema.


Ndipo akachimwa munthu mmodzi osati dala, abwere nayo mbuzi yaikazi ya chaka chimodzi, ikhale nsembe yauchimo.


koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwanawankhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa