Ndipo ulikute ndi golide woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolide pozungulira pake.
Eksodo 25:12 - Buku Lopatulika Ndipo uliyengere mphete zinai zagolide, ndi kuziika kumiyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziwiri pa ina. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo uliyengere mphete zinai zagolide, ndi kuziika kumiyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziwiri pa ina. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Upange mphete zinai zagolide zonyamulira bokosilo, ndi kumangirira mphetezo ku miyendo yake inai, uku ziŵiri uku ziŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Upange mphete zinayi zagolide ndipo uzimangirire ku miyendo yake inayi ya bokosilo, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri. |
Ndipo ulikute ndi golide woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolide pozungulira pake.
Nulipangire mphete zinai zagolide, ndi kuika mphetezo pangodya zinai zokhala pa miyendo yake inai.
Ndipo uzikuta matabwa ndi golide, ndi kupanga mphete zao zagolide zopisamo mitandayo; uzikutanso mitandayo ndi golide.
Ndipo apise mphiko m'mphetezo kuti mphikozo zikhale pa mbali ziwiri za guwa la nsembe polinyamula.
Ndipo anapisa mphiko m'mphetezo pa mbali zake za likasalo, kuti anyamulire nazo likasa.
Ndipo anapisa mphikozo mu mphetezo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere.
Anapanganso zoikamo ziwiri zagolide, ndi mphete ziwiri zagolide; naika mphete ziwirizo pansonga ziwiri za chapachifuwa.