ndi kubwera nazo zipatso zoyamba za nthaka, ndi zoyamba za zipatso zonse za mtengo uliwonse chaka ndi chaka, ku nyumba ya Yehova;
Eksodo 23:19 - Buku Lopatulika Uzibwera nazo zoyambayamba za m'munda mwako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwanawambuzi mu mkaka wa make. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Uzibwera nazo zoyambayamba za m'munda mwako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwanawambuzi mu mkaka wa make. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Muzibwera ndi zokolola zoyamba zabwino kwambiri za kumunda kwanu ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu. “Musamaphika kamwanakanyama mu mkaka wa make. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku Nyumba ya Yehova Mulungu wanu. “Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake. |
ndi kubwera nazo zipatso zoyamba za nthaka, ndi zoyamba za zipatso zonse za mtengo uliwonse chaka ndi chaka, ku nyumba ya Yehova;
ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'chilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu;
Usachedwa kuperekako zipatso zako zochuluka, ndi zothira zako. Woyamba wa ana ako aamuna undipatse Ine.
Uzibwera nazo zipatso zoyambayamba za nthaka yako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.
Pakuti miyambo ya anthu ili yachabe, pakuti wina adula mtengo m'nkhalango, ntchito ya manja a mmisiri ndi nkhwangwa.
Ndi zoyamba za zipatso zoyamba za zinthu zilizonse, ndi nsembe zokweza zilizonse za nsembe zanu zonse zokweza nza ansembe; muperekenso ufa wanu woyamba kwa wansembe, kuti mdalitso ukhalebe pa nyumba yako.
Ndipo polingana ndi malire a ansembe Alevi akhale nalo gawo la mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi mikono zikwi khumi kupingasa kwake; m'litali mwake monse ndimo mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwake mikono zikwi khumi.
Ndipo asagulitseko, kapena kulisintha, kapena kupitiriza zipatso zoyamba za dziko; pakuti lili lopatulika la Yehova.
Musamadya chinthu chilichonse chitafa chokha; muzipereka icho kwa mlendo ali m'mudzi mwanu, achidye ndiye; kapena uchigulitse kwa mlendo; popeza ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu. Musamaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.
Ndipo tsopano, taonani, ndabwera nazo zoyamba za zipatso za nthaka, zimene Inu, Yehova, mwandipatsa. Ndipo muziike pamaso pa Yehova Mulungu wanu;
kuti muzitengako zoyamba za zipatso zonse za nthaka, zakubwera nazo inu zochokera m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndi kuziika mudengu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.
Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoyamba kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.