Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova; akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova.
Eksodo 23:17 - Buku Lopatulika Katatu m'chaka amuna onse azioneka pamaso pa Ambuye Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Katatu m'chaka amuna onse azioneka pamaso pa Ambuye Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu aamuna onse aziwonekera pamaso pa Ine Chauta pa masiku atatu ameneŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Amuna onse azionekera pamaso pa Ambuye Yehova katatu pa chaka. |
Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova; akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova.
Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo. Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?
Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?
Amuna ako onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, katatu chaka chimodzi.
Pakudzaonekera inu pamaso pa Ine, ndani wafuna chimenechi m'dzanja lanu, kupondaponda m'mabwalo mwanga?
Ndipo pamene Iye anakhala ndi zaka zake khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga machitidwe a chikondwerero;
Koma kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mafuko anu onse kuikapo dzina lake, ndiko ku chokhalamo chake, muzifunako, ndi kufikako;
Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;
pakufika Israele wonse kuoneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene adzasankha, muzilalikira chilamulo ichi pamaso pa Israele wonse, m'makutu mwao.