Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 23:14 - Buku Lopatulika

14 Muzindichitira Ine madyerero katatu m'chaka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Muzindichitira Ine madyerero katatu m'chaka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 “Muzikhala ndi tsiku lachikondwerero katatu pa chaka, kuti mundilemekeze Ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 “Muzichita zikondwerero zolemekeza Ine katatu pa chaka.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 23:14
14 Mawu Ofanana  

Ndipo chaka chimodzi Solomoni anapereka katatu nsembe zopsereza ndi zamtendere, paguwa la nsembe limene anammangira Yehova, nafukiza zonunkhira paguwa la nsembe pamaso pa Yehova, atatsiriza nyumbayo.


monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika, katatu m'chaka: pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, ndi pa chikondwerero cha Masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa.


Katatu m'chaka amuna onse azioneka pamaso pa Ambuye Yehova.


Usadzipangire milungu yoyenga.


Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka mu Ejipito.


Koma pofika anthu a m'dziko pamaso pa Yehova m'zikondwerero zoikika, iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumpoto kudzalambira, atulukire njira ya kuchipata cha kumwera; ndi iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumwera, atulukire njira ya kuchipata cha kumpoto; asabwerere njira ya chipata anadzeracho, koma atulukire m'tsogolo mwake.


muwerenge masiku makumi asanu kufikira tsiku lotsata sabata lachisanu ndi chiwiri; pamenepo mubwere nayo kwa Yehova nsembe ya ufa watsopano.


Nena ndi ana a Israele, kuti, Tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uno wachisanu ndi chiwiri pali chikondwerero cha Misasa ya Yehova, masiku asanu ndi awiri.


Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, misonkhano yopatulika, zimene muzilalikira pa nyengo zoikika zao.


Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, pali Paska wa Yehova.


Samalirani mwezi wa Abibu, kuti muzichitira Yehova Mulungu wanu Paska; popeza m'mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani m'dziko la Ejipito usiku.


Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;


Ndipo munthuyo akakwera chaka ndi chaka kutuluka m'mzinda mwake kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Yehova wa makamu mu Silo. Ndipo pomwepo panali ana aamuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Finehasi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa