Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panatuluka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Saulo, dzina lake ndiye Simei, mwana wa Gera; iyeyu anatulukako, nayenda natukwana.
Eksodo 22:27 - Buku Lopatulika popeza chofunda chake ndi ichi chokha, ndicho chovala cha pathupi pake; azifundira chiyani pogona? Ndipo kudzakhala kuti akandifuulira Ine, ndidzamva; pakuti Ine ndine wachisomo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 popeza chofunda chake ndi ichi chokha, ndicho chovala cha pathupi pake; azifundira chiyani pogona? Ndipo kudzakhala kuti akandifuulira Ine, ndidzamva; pakuti Ine ndine wachisomo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa poti chofunda nchokhacho, ndicho chotetezera thupi lake. Nanga adzafunda chiyani? Akalira kwa Ine iyeyu kuti ndimthandize, ndidzamuyankha chifukwa ndine wachifundo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero chifukwa chovala chimene amadzifundira nacho nʼchomwecho. Nanga usiku adzafunda chiyani? Tsonotu ngati adzandilirira, Ine ndidzamva pakuti ndine wachifundo. |
Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panatuluka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Saulo, dzina lake ndiye Simei, mwana wa Gera; iyeyu anatulukako, nayenda natukwana.
Ndipo taona uli naye Simei mwana wa Gera wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikulu tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordani, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga.
Ndipo tsono, usamuyesera iye wosachimwa, popeza ndiwe munthu wanzeru, ndipo udziwa umo uyenera kumchitira iye, nutsitsire mutu wake waimvi ndi mwazi kumanda.
Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza chifundo pamaso pa iwo anawatenga ndende, nadzalowanso m'dziko muno; pakuti Yehova Mulungu wanu ngwa chisomo ndi chifundo; sadzakuyang'anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye.
Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.
Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.
Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang'ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwao;
Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi;
Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'chipinda chogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo chouluka ndi mapiko chidzamveketsa zonenazo.
Ndipo chidzakhala chizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m'dziko la Ejipito; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, chifukwa cha osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa.
Mukakongoletsa mnansi wanu ngongole iliyonse, musamalowa m'nyumba mwake kudzitengera chikole chake.