Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 10:20 - Buku Lopatulika

20 Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'chipinda chogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo chouluka ndi mapiko chidzamveketsa zonenazo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'chipinda chogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo chouluka ndi mapiko chidzamveketsa zonenazo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Ngakhale mumtima mwako usamainyoza mfumu. Ngakhale m'chipinda mwako momwe usamatukwana wolemera. Mwina kambalame kamumlengalenga kapena kachilombo kena kouluka nkukumvera, kenaka nkukaulula zonse kwa amene umaŵanenawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Usanyoze mfumu ngakhale mu mtima mwako, kapena kutukwana munthu wachuma mʼchipinda chako, pakuti mbalame yamlengalenga itha kutenga mawu ako nʼkukafotokoza zomwe wanena.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 10:20
11 Mawu Ofanana  

Nati mmodzi wa anyamata ake, Iai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israele ndiye amafotokozera mfumu ya Israele mau muwanena m'kati mwake mwa chipinda chanu chogonamo.


Koma chidadziwika ichi kwa Mordekai, ndiye anafotokozera Estere mkazi wamkulu; ndi Estere anamuuza mfumu, kumnenera Mordekai.


popeza chofunda chake ndi ichi chokha, ndicho chovala cha pathupi pake; azifundira chiyani pogona? Ndipo kudzakhala kuti akandifuulira Ine, ndidzamva; pakuti Ine ndine wachisomo.


Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkulu wa anthu a mtundu wako.


ndipo m'mtsinjemo mudzachuluka achule, amene adzakwera nadzalowa m'nyumba mwako, ndi m'chipinda chogona iwe, ndi pakama pako, ndi m'nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m'michembo yanu yootcheramo, ndi m'mbale zanu zoumbiramo.


Ndipo iwo adzapitirira ovutidwa ndi anjala, ndipo padzakhala kuti pokhala ndi njala iwo adzadziputa okha, ndi kutemberera mfumu yao, ndi Mulungu wao; ndi kugadamira nkhope zao kumwamba;


Koma Marita anatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo anadzako nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize.


Ndipo anayankha nati, Ndinena ndi inu, ngati awa khala chete miyala idzafuula.


Ndipo Paulo anati, Sindinadziwe, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera choipa mkulu wa anthu ako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa