Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.
Eksodo 2:22 - Buku Lopatulika Ndipo anaona mwana, ndi Mose anamutcha dzina lake Geresomo; pakuti anati, Ndakhala mlendo m'dziko la eni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaona mwana, ndi Mose anamutcha dzina lake Geresomo; pakuti anati, Ndakhala mlendo m'dziko la eni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zipora adabala mwana wamwamuna. Pamenepo Mose adati, “Ndine mlendo m'dziko lachilendo.” Motero adamutcha mwanayo Geresomo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zipora anabereka mwana wa mwamuna amene Mose anamutcha Geresomu, popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko la eni.” |
Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.
nayendayenda kuchokera mtundu wina kufikira mtundu wina, kuchokera ufumu wina kufikira anthu ena.
Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.
Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo tcherani khutu kulira kwanga; musakhale chete pa misozi yanga; Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu, wosakhazikika, monga makolo anga onse.
Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake. Ndipo anamutcha dzina lake Mose, nati, Chifukwa ndinamvuula m'madzi.
Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, nawakweza pabulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lake.
Ndipo asaligulitse dziko chigulitsire; popeza dzikoli ndi langa; pakuti inu ndinu alendo akugonera ndi Ine.
Ndipo Mose anathawa pa mau awa, nakhala mlendo m'dziko la Midiyani; kumeneko anabala ana aamuna awiri.
Ndipo ana a Dani anadziimitsira fano losemalo; ndi Yonatani mwana wa Geresomo mwana wa Manase, iye ndi ana ake aamuna anali ansembe a fuko la Adani mpaka tsiku lija anatenga ndende anthu a m'dziko.
Ndipo panali pamene nthawi yake inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Samuele, nati, Chifukwa ndinampempha kwa Yehova,