Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 39:12 - Buku Lopatulika

12 Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo tcherani khutu kulira kwanga; musakhale chete pa misozi yanga; Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu, wosakhazikika, monga makolo anga onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo tcherani khutu kulira kwanga; musakhale chete pa misozi yanga; Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu, wosakhazikika, monga makolo anga onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Mverani pemphero langa, Inu Chauta, mumve kulira kwanga. Musakhale chete pamene ndikulirira Inu. Ndine mlendo wanu wosakhalitsa, munthu wongokhala nawo monga adaachitira makolo anga onse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Imvani pemphero langa Inu Yehova, mverani kulira kwanga kopempha thandizo; musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu, popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa; monga anachitira makolo anga onse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 39:12
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anakhala ngati mlendo masiku ambiri m'dziko la Afilisti.


Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.


Kapena Yehova adzayang'anira chosayenerachi alikundichitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera chabwino m'malo mwa kunditukwana kwa lero.


Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova.


Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.


Momwemo munthu akutha ngati chinthu choola, ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.


Mabwenzi anga andinyoza; koma diso langa lilirira misozi kwa Mulungu.


Yehova, imvani pemphero langa, ndipo mfuu wanga ufikire Inu.


Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.


Ine ndine mlendo padziko lapansi; musandibisire malamulo anu.


Malemba anu anakhala nyimbo zanga m'nyumba ya ulendo wanga.


Muwerenga kuthawathawa kwanga, sungani misozi yanga m'nsupa yanu; kodi siikhala m'buku mwanu?


Pakuti masiku athu onse apitirira mu ukali wanu; titsiriza moyo wathu ngati lingaliro.


Ndipo asaligulitse dziko chigulitsire; popeza dzikoli ndi langa; pakuti inu ndinu alendo akugonera ndi Ine.


Pokhala nako kulimbika mtima nthawi zonse tsono, ndipo podziwa kuti pamene tili kwathu m'thupi, sitili kwa Ambuye.


Iwo onse adamwalira m'chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Ndipo mukamuitana ngati Atate, Iye amene aweruza monga mwa ntchito ya yense, wopanda tsankho, khalani ndi mantha nthawi ya chilendo chanu;


Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa