Ndipo Yehova anatsikira paphiri la Sinai, pamutu pake paphiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu paphiri; ndi Mose anakwerapo.
Eksodo 19:3 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adakwera phiri kukakumana ndi Mulungu, ndipo Mulungu adamuitana m'phirimo namuuza kuti, “Uuze zidzukulu za Yakobe, ndiye kuti mtundu wonse wa Aisraele kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anakwera ku phiri kukakumana ndi Mulungu ndipo Yehova anamuyitana nati, “Ukawuze zidzukulu za Yakobo, ana onse a Israeli kuti, |
Ndipo Yehova anatsikira paphiri la Sinai, pamutu pake paphiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu paphiri; ndi Mose anakwerapo.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo ndawalembera kuti uwalangize.
Ndipo Iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo mu Ejipito, mudzatumikira Mulungu paphiri pano.
Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m'kati mwa chitsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndili pano.
Nukonzekeretu m'mawa, nukwere m'mawa m'phiri la Sinai, nuimepo pamaso panga pamwamba paphiri.
Ndipo anasema magome awiri a miyala, onga oyamba aja; ndipo Mose anauka mamawa nakwera m'phiri la Sinai, monga Yehova adamuuza, nagwira m'dzanja mwake magome awiri amiyala.
Uyu ndiye amene anali mu Mpingo m'chipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m'phiri la Sinai, ndi makolo athu: amene analandira maneno amoyo akutipatsa ife;